Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 56:1 - Buku Lopatulika

1 Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mundichitire chifundo, Mulungu, pakuti anthu afuna kundimeza. Andipsinja pondithira nkhondo tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti anthu akundizunza. Adani akundithira nkhondo ndi kundipsinja tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri; tsiku lonse akundithira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 56:1
25 Mawu Ofanana  

Dziko lidayasama nilidameza Datani, ndipo linafotsera gulu la Abiramu.


Akadatimeza amoyo, potipsera mtima wao.


Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba; pakuti chifundo chake nchosatha.


Nakhuthula Farao ndi khamu lake mu Nyanja Yofiira: pakuti chifundo chake nchosatha.


Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga, ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga; pakuti ine ndine mtumiki wanu.


Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.


Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa.


Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.


Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine. Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mavuto.


Asanene mumtima mwao, Hede, momwemo! Asanene, Tammeza iye.


Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi?


Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga, ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira.


Mulungu wa chifundo changa adzandichingamira, adzandionetsa tsoka la adani anga.


Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni.


tiwameze ali ndi moyo ngati manda, ali amphumphu, ngati akutsikira kudzenje;


Adani ako onse ayasamira pa iwe, atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza; ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.


Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.


Ambuye wasanduka mdani, wameza Israele; wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake; nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.


Israele wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati chotengera choti munthu sakondwera nacho.


Ndipo pamene chovunda ichi chikadzavala chisavundi ndi chaimfa ichi chikadzavala chosafa, pamenepo padzachitika mau olembedwa, Imfayo yamezedwa m'chigonjetso.


Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa