Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 56:2 - Buku Lopatulika

2 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse, pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Adani anga afuna kundimeza tsiku lonse, pakuti ambiri andithira nkhondo modzikuza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adani akundizunza tsiku lonse, pali ambiri amene akumenyana nane monyada.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse, ambiri akumenyana nane monyada.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 56:2
16 Mawu Ofanana  

Yehova! Ha! Achuluka nanga akundisautsa ine! Akundiukira ine ndi ambiri.


Tsutsanani nao iwo akutsutsana nane, Yehova; limbanani nao iwo akulimbana nane.


Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?


Adzabwezera choipa adani anga, aduleni m'choonadi chanu.


Adzanditumizira m'mwamba, nadzandipulumutsa ponditonza wofuna kundimeza; Mulungu adzatumiza chifundo chake ndi choonadi chake.


Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Nkokoma kuyamika Yehova, ndi kuimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.


Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba kunthawi yonse.


Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, ndi mafunde olimba a nyanja.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Mfumu inu, Mulungu Wam'mwambamwamba anapatsa Nebukadinezara atate wanu ufumuwu, ndi ukulu, ndi ulemerero, ndi chifumu;


Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi?


pakuti ali mizimu ya ziwanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kunka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa