Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 1:9 - Buku Lopatulika

9 koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndithu m'mitima mwathu tinkangoganiza kuti basi talandira chilango chokaphedwa. Zimenezi zidachitika kuti tisamadzikhulupirire, koma kuti tizikhulupirira Mulungu amene amaukitsa akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 1:9
20 Mawu Ofanana  

Pamenepo inenso ndidzakuvomereza, kuti dzanja lakolako lamanja likupulumutsa.


Onenepa onse a padziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.


Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.


Wokhulupirira mtima wakewake ali wopusa; koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.


Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.


Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama chilungamo chake, akachita chosalungama, sizikumbukika zolungama zake zilizonse; koma m'chosalungama chake anachichita momwemo adzafa.


Ndipo anatinso kwa ena amene anadzikhulupirira mwa iwo okha kuti ali olungama, napeputsa onse ena, fanizo ili,


Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha.


amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;


Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho mu Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;


si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;


Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife;


poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kuchokera komwe, pachiphiphiritso, anamlandiranso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa