Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 1:8 - Buku Lopatulika

8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho mu Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za chisautso chathu tinakomana nacho m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukulu, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono abale, tifuna kuti mudziŵe, masautso amene tidakumana nawo ku dziko la Asiya, adatipsinja koopsa, kopitirira mphamvu zathu, kotero kuti sitinkayembekezanso kuti nkukhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 1:8
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;


Ndipo pamene ananena izi, anamasula msonkhano.


Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;


Ndipo sindifuna kuti inu, abale, mudzakhala osadziwa, kuti kawirikawiri ndikanena mumtima kuti ndikafike kwa inu, koma ndaletsedwa kufikira lero, kuti ndikaone zobala zina mwa inunso, monga mwa anthu amitundu ena.


Ngati ndinalimbana ndi zilombo ku Efeso monga mwa munthu, ndipindulanji? Ngati akufa saukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.


Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.


Mwadzala kale, mwalemerera kale, mwachita ufumu opanda ife; ndipo mwenzi muchitadi ufumu, kuti ifenso tikachite ufumu pamodzi ndi inu.


koma tokha tinakhala nacho chitsutso cha imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;


monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani tili ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;


Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.


Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa