Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 17:8 - Buku Lopatulika

8 Ndisungeni monga kamwana ka m'diso, ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndisungeni monga kamwana ka m'diso, ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mundisunge ngati mwana wa diso, munditeteze pansi pa mapiko anu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mundisunge ine ngati mwanadiso; mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 17:8
16 Mawu Ofanana  

Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.


Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.


Adzakhuta kwambiri ndi zonona za m'nyumba mwanu, ndipo mudzawamwetsa mu mtsinje wa zokondweretsa zanu.


Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.


Ndidzafuulira kwa Mulungu Wam'mwambamwamba; ndiye Mulungu wonditsirizira zonse.


Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.


Pakuti Inu, Mulungu, mudamva zowinda zanga; munandipatsa cholowa cha iwo akuopa dzina lanu.


Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.


Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.


Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m'mapiko ake, koma inu simunafune ai!


Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneri, ndi wakuponya miyala iwo atumidwa kwa iwe! Ha! Kawirikawiri ndinafuna kusonkhanitsa ana ako, monga ngati thadzi ndi anapiye ake m'mapiko ake, ndipo simunafunai!


Anampeza m'dziko la mabwinja, m'chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m'diso.


Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa