Masalimo 60 - Buku LopatulikaMadandaulo ndi pempho la Davide Kwa Mkulu wa Nyimbo: pa Susan-Eduti. Mikitamu wa Davide; lakulangiza; muja analimbana nao Aramu Naharaimu ndi Aramu Zoba, nabwera Yowabu anapha a Edomu kuchigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu ziwiri. 1 Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni. 2 Mwagwedeza dziko, mwaling'amba. Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka. 3 Mwaonetsa anthu anu zowawa, mwatimwetsa vinyo wotinjenjemeretsa. 4 Koma mwapatsa mbendera akuopa Inu, aikweze chifukwa cha choonadi. 5 Kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze. 6 Mulungu walankhula m'chiyero chake; ndidzakondwerera, ndidzagawa Sekemu, ndidzayesa muyeso chigwa cha Sukoti. 7 Giliyadi ndi wanga, Manasenso ndi wanga; ndipo Efuremu ndi mphamvu ya mutu wanga; Yuda ndiye wolamulira wanga. 8 Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine. 9 Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu? 10 Si ndinu, Mulungu, amene mwatitaya? Osatuluka nao makamu athu, Mulungu. 11 Tithandizeni kunsautso; kuti chipulumutso cha munthu ndi chabe. 12 Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima, ndipo Iye adzapondereza otisautsa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi