Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.
Eksodo 15:11 - Buku Lopatulika Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndithu Yehova, pakati pa milungu, ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera, ndiponso wotamandika wolemekezeka, chifukwa cha ntchito zanu, zazikulu ndi zodabwitsa? |
Chifukwa chake wamkulu ndi Inu Yehova Mulungu, pakuti palibe wina wofanana ndi Inu, palibe Mulungu winanso koma Inu, monga mwa zonse tinazimva ndi makutu athu.
Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu wolingana ndi Inu m'thambo la kumwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,
Pakuti Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Ndipo nyumba nditi ndimangeyi ndi yaikulu; pakuti Mulungu wathu ndiye wamkulu woposa milungu yonse.
nati, Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu ngati Inu, m'mwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse;
Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Ndidzakumbukira zimene adazichita Yehova; inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zoyambira kale.
Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa; munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.
Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.
Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka.
Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu.
Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pamadzi a mu Ejipito; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Ejipito.
Pakuti nthawi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine padziko lonse lapansi.
Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani?
Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina wofanana ndi Ine;
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.
Gawo la Yakobo silifanana ndi iwo; pakuti Iye ndiye analenga zonse; Israele ndiye mtundu wa cholowa chake; dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wochokera ku Yordani wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amchokere; ndipo aliyense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wake, pakuti wakunga Ine ndani? Adzandiikira nthawi ndani? Ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?
Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.
Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.
Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.
Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu;
Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena padziko lapansi wakuchita monga mwa ntchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?
Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe, wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza, ndi pa mitambo mu ukulu wake.
Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?
ndipo analambira chinjoka, chifukwa chinachipatsa ulamuliro chilombocho; ndipo analambira chilombo ndi kunena, Afanana ndi chilombo ndani? Ndipo akhoza ndani kumenyana nacho nkhondo?
Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.
Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.
Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.