Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 15:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndithu Yehova, pakati pa milungu, ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera, ndiponso wotamandika wolemekezeka, chifukwa cha ntchito zanu, zazikulu ndi zodabwitsa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 15:11
51 Mawu Ofanana  

Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu.


nati: “Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pansi pa dziko, inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse.


Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda; Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.


“Nyumba ya Mulungu imene ndidzamange idzakhala yayikulu, chifukwa Mulungu wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.


Iye anati, “Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pa dziko. Inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse.


Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu, Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?


Thupi langa limanjenjemera chifukwa cha kuopa Inu; ndimachita mantha ndi malamulo anu.


Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.


Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse, ndi wokonda zonse zimene anazipanga.


Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni! Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni! Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!


Thupi langa lidzafuwula mokondwera, “Ndani angafanane nanu Yehova? Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri, osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”


Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba, konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.


Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.


Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova; Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.


Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa; Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.


Njira yanu inadutsa pa nyanja, njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu, ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.


Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndiye Mulungu.


Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye; palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.


Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova, Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.


Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu? Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.


Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.”


“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.”


Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite.


Farao anati, “Mawa.” Mose anamuyankha kuti, “Chabwino zidzakhala monga mwaneneramu, kuti mudzadziwe kuti palibe wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu.


Kotero Aaroni analoza dzanja lake pa madzi a ku Igupto, ndipo achule anatuluka nadzaza dziko lonse la Igupto.


Ngati suwalola, tsopano ndidzagwetsa miliri yanga yonse pa iwe ndi nduna zako ndiponso pa anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wina wofanana nane pa dziko lonse lapansi.


Patukani pa njira ya Yehova, lekani kutsata njira ya Yehova; ndipo tisamvenso mawu a Woyerayo uja wa Israeli!”


Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani?


Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani? Kapena kodi alipo wofanana nane?”


Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana; chifukwa Ine ndine Mulungu ndipo palibe wina ofanana nane.


Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.


Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”


Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo. Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake. Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.


“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani kupita ku malo a msipu wobiriwira, Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo. Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine. Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani? Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”


“Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.


Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.


Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye.


Yehova Mulungu wanu, amene akukutsogolerani, adzakumenyerani nkhondo monga muja anachitira ku Igupto inu mukuona,


“Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita?


“Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni, amene amakwera pa thambo kukuthandizani ndiponso pa mitambo ya ulemerero wake.


Kodi alipo mulungu amene anayeserapo kudzitengera mtundu wa anthu kuwachotsa mu mtundu unzake mwa mayesero, zizindikiro zozizwitsa, nkhondo, komanso mwa mphamvu zake zopanda malire, kapena mwa zochita zazikulu ndi zochititsa mantha, monga zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Igupto inu mukupenya?


Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”


Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani, ndi kulemekeza dzina lanu? Pakuti Inu nokha ndiye woyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzapembedza pamaso panu, pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”


Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti, “Woyera, woyera, woyera ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.”


“Palibe wina woyera ngati Yehova, palibe wina koma inu nokha, palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa