Eksodo 9:14 - Buku Lopatulika14 Pakuti nthawi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine padziko lonse lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Pakuti nthawi yino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine pa dziko lonse lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Tsopano ndikuti ndigwetsere miliri yanga yonse pa iwe, pa nduna zako, ndi pa anthu ako, ndipo udzadziŵa kuti palibe wina aliyense wofanafana ndi Ine pa dziko lonse lapansi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Ngati suwalola, tsopano ndidzagwetsa miliri yanga yonse pa iwe ndi nduna zako ndiponso pa anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wina wofanana nane pa dziko lonse lapansi. Onani mutuwo |
ndipo anamuinga kumchotsa kwa ana a anthu, ndi mtima wake unasandulika ngati wa nyama zakuthengo, ndi pokhala pake mpa mbidzi, anamdyetsa udzu ngati ng'ombe, ndi thupi lake linakhathamira ndi mame a kumwamba; mpaka anadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, nauikira aliyense Iye afuna mwini.