Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 15:4 - Buku Lopatulika

4 Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani, ndi kulemekeza dzina lanu? Pakuti Inu nokha ndiye woyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzapembedza pamaso panu, pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 15:4
44 Mawu Ofanana  

Iye ndiye Yehova, Mulungu wathu; maweruzo ake akhala padziko lonse lapansi.


Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.


Inu akuopa Yehova, mumlemekeze; inu nonse mbumba ya Yakobo, mumchitire ulemu; ndipo muchite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israele.


Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Koma Inu ndinu woyera, wakukhala m'malemekezo a Israele.


Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; nadzalemekeza dzina lanu.


Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.


Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana aakazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.


Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani poponderapo mapazi ake: Iye ndiye Woyera.


Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo gwadirani paphiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.


Chifukwa chake lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israele, m'zisumbu za m'nyanja.


Chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mzinda wa mitundu yakuopsa udzakuopani Inu.


Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.


Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Ndipo wina anafuula kwa mnzake, nati, Woyera, Woyera, Woyera, Yehova wa makamu; dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.


Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.


Wosaopa Inu ndani, Mfumu ya amitundu? Pakuti kukuopani ndi kwanu; pakuti mwa anzeru onse a amitundu, ndi m'maufumu ao onse, mulibe akunga Inu.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.


atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


Ndipo kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga chikondwerero cha Misasa.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu.


popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.


Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, chifukwa mudaweruza kotero;


Ndipo ndinamva wa paguwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.


pakuti maweruzo ake ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.


Ndipo anampatsa iye avale bafuta wonyezimira woti mbuu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Filadelfiya lemba: Izi anena Iye amene ali Woyera, Iye amene ali Woona, Iye wakukhala nacho chifungulo cha Davide, Iye wotsegula, ndipo palibe wina atseka; Iye wotseka, ndipo palibe wina atsegula:


Ndipo zamoyozo zinai, chonse pa chokha chinali nao mapiko asanu ndi limodzi; ndipo zinadzala ndi maso pozinga ponse ndi m'katimo; ndipo sizipumula usana ndi usiku, ndi kunena, Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.


ndipo anafuula ndi mau aakulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?


Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa