Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 90:11 - Buku Lopatulika

11 Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani, ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani, ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Kodi ndani amadziŵa kukula kwa mkwiyo wanu ndi ukali wanu, kupambana anthu okuwopani?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu? Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 90:11
12 Mawu Ofanana  

Inu ndinu woopsa; ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala chilili ndani pamaso panu?


Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?


Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.


Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.


Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zoipa zanu.


Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.


Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.


Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya ku Gehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.


Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu.


Yehova adzachita miliri yanu ndi ya ana anu ikhale yodabwitsa, miliri yaikulu ndi yokhalitsa, ndi nthenda zoipa ndi zokhalitsa.


chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa