Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 19:2 - Buku Lopatulika

2 Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nena ndi khamu lonse la ana a Israele, nuti nao, Muzikhala oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, ndine woyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Uza mpingo wonse wa Aisraele kuti, ‘Mukhale oyera pakuti Ine Chauta, Mulungu wanu, ndine woyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 19:2
20 Mawu Ofanana  

Alemekeze dzina lanu lalikulu ndi loopsa. Ili ndilo loyera.


ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.


Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.


Chifukwa chake dzipatuleni, nimukhale oyera; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.


koma asafike ku nsalu yotchinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali nacho chilema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.


Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.


Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu?


Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.


Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.


monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.


Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino.


Ndipo Yoswa anati kwa anthu, Simungathe inu kutumikira Yehova pakuti ndiye Mulungu woyera, ndi Mulungu wansanje; sadzalekerera zolakwa zanu, kapena zochimwa zanu.


Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa