Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 13:4 - Buku Lopatulika

4 ndipo analambira chinjoka, chifukwa chinachipatsa ulamuliro chilombocho; ndipo analambira chilombo ndi kunena, Afanana ndi chilombo ndani? Ndipo akhoza ndani kumenyana nacho nkhondo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ndipo analambira chinjoka, chifukwa chinachipatsa ulamuliro chilombocho; ndipo analambira chilombo ndi kunena, Afanana ndi chilombo ndani? Ndipo akhoza ndani kugwira nkhondo nacho?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adachipembedza chinjoka chija chifukwa chidaapatsa ulamuliro wake kwa chilombo chija. Nachonso chilombo chija adachipembedza nkumanena kuti, “Ndani angafanane ndi chilombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 13:4
18 Mawu Ofanana  

Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?


Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?


mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.


anthu aakulu ndi ataliatali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?


amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.


Ndipo chinaoneka chizindikiro china m'mwamba taonani, chinjoka chofiira, chachikulu, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pake nduwira zachifumu zisanu ndi ziwiri.


Ndipo mchira wake uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala icho chikalikwire mwana wake.


Ndipo ndinaona chilombo china chilikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziwiri ngati za mwanawankhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka.


Ndipo anachipatsa mphamvu yakupatsa fano la chilombo mpweya, kutinso fano la chilombo lilankhule, nilichite kuti onse osalilambira fano la chilombo aphedwe.


Ndipo chilombo ndinachionacho chinafanana ndi nyalugwe, ndi mapazi ake ngati mapazi a chimbalangondo, ndi pakamwa pake ngati pakamwa pa mkango; ndipo chinjoka chinampatsa iye mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.


Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawagonjetsa, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.


nafuula poona utsi wa kutentha kwake, nanena, Mzinda uti ufanana ndi mzinda waukuluwo?


Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;


Ndipo Aisraele onse, pakumuona munthuyo, anamthawa, naopa kwambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa