Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo.
2 Samueli 5:7 - Buku Lopatulika Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mzinda wa Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mudzi wa Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe Davide adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide. |
Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo.
Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.
Momwemo Davide sanafune kudzitengera likasa la Yehova lidze kumzinda wa Davide; koma Davide analipambutsira kunyumba ya Obededomu Mgiti.
Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumzinda wa Davide, ali ndi chimwemwe.
Ndipo kunali pamene likasa la Yehova linafika m'mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kusewera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.
Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.
Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni mu Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mzinda wa Davide, ndiwo Ziyoni.
Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mzinda wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.
Ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino mu Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake.
Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova kumzinda wa Davide ndiwo Ziyoni.
Ndi Chipata cha ku Kasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pamunda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumzinda wa Davide.
Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova.
Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?
Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.
monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.
Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,
Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.