Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 48:3 - Buku Lopatulika

3 Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mulungu waonetsa kuti ndiye woteteza mzindawo, pakuti Iye amakhala m'kati mwa malinga ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mulungu ali mu malinga ake; Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 48:3
14 Mawu Ofanana  

Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mzinda wa Davide.


Ndipo pamene Yehova anaona kuti anadzichepetsa, mau a Yehova anadza kwa Semaya, ndi kuti, Anadzichepetsa; sindidzawaononga; koma katsala kanthawi ndipo ndidzawapatsa chipulumutso, wosatsanulira mkwiyo wanga pa Yerusalemu ndi dzanja la Sisake.


Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.


Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni, amene akhala mu Yerusalemu. Aleluya.


Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Mulungu awalira mu Ziyoni, mokongola mwangwiro.


Wakongola, bwenzi langa, namwaliwe ngati Tiriza, wokoma ngati Yerusalemu, woopsa ngati nkhondo ndi mbendera.


Onse opita panjira akuombera manja: Atsonya, napukusira mitu yao pa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati, kodi uwu ndi mzinda wotchedwa wokongola, wangwiro, wokondweretsa dziko lonse?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa