Masalimo 48 - Buku LopatulikaUkoma ndi ulemerero wa Ziyoni Nyimbo. Salimo la ana a Kora. 1 Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera. 2 Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu. 3 Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje. 4 Pakuti, taonani, mafumuwo anasonkhana, anapitira pamodzi. 5 Anapenya mudziwo, ndipo pamenepo anadabwa; anaopsedwa, nathawako. 6 Pomwepo anagwidwa nako kunthunthumira; anamva chowawa, ngati wam'chikuta. 7 Muswa zombo za ku Tarisisi ndi mphepo ya kum'mawa. 8 Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mzinda wa Yehova wa makamu, m'mzinda wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya. 9 Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu, m'kati mwa Kachisi wanu. 10 Monga dzina lanu, Mulungu, momwemo lemekezo lanu ku malekezero a dziko lapansi; m'dzanja lamanja lanu mudzala chilungamo. 11 Likondwere phiri la Ziyoni, asekere ana aakazi a Yuda, chifukwa cha maweruzo anu. 12 Zungulirani Ziyoni, ndipo muuzinge, werengani nsanja zake. 13 Penyetsetsani malinga ake, yesetsani zinyumba zake; kuti mukaziwerengere mibadwo ikudza m'mbuyo. 14 Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi