Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 48:8 - Buku Lopatulika

8 Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mzinda wa Yehova wa makamu, m'mzinda wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Monga tidamva, momwemo tidapenya m'mudzi wa Yehova wa makamu, m'mudzi wa Mulungu wathu, Mulungu adzaukhazikitsa kunthawi yamuyaya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Zimene ife tidazimva, taziwona zomwezo mu mzinda wa Chauta Wamphamvuzonse, mzinda wa Mulungu wathu, umene adaukhazikitsa mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Monga momwe tinamvera, kotero ife tinaona mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse, mu mzinda wa Mulungu wathu. Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 48:8
11 Mawu Ofanana  

Pamenepo Ahaziya mwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana.


Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika, Mulungu adzauthandiza mbandakucha.


Ndipo adzanena za Ziyoni, uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo; ndipo Wam'mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa.


Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.


Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.


Opalasa ako anakufikitsa kumadzi aakulu; mphepo ya kum'mawa inakuthyola m'kati mwa nyanja.


Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.


Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa