1 Mafumu 3:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumudzi wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Solomoni adapalana chibwenzi ndi Farao mfumu ya ku Ejipito pokwatira mwana wa Faraoyo. Adabwera naye mkaziyo ku mzinda wa Davide ku Yerusalemu, nakhala naye komweko mpaka atamaliza kumanga nyumba yake yatsopano ndi Nyumba ya Chauta ndiponso linga lozungulira mzindawo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu. Onani mutuwo |