Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 21:13 - Buku Lopatulika

13 Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 “ ‘Ndikukuimbani mlandu, inu anthu okhala m'chigwa inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,’ ” akutero Chauta. “Inu amene mumati, ‘Ndani angatithire nkhondo? Ndani angathe kuloŵa m'malinga mwathu?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndidzalimbana nanu, inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa, inu okhala ngati thanthwe lapachidikha, akutero Yehova. Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe? Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 21:13
21 Mawu Ofanana  

Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


Ndipo anachokera ku Sukoti, nagona ku Etamu, pa malekezero a chipululu.


Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine mu Ejipito.


Katundu wa chigwa cha masomphenya. Mwatani kuti mwakwera nonsenu pamatsindwi?


Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka chuma chako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, chifukwa cha tchimo, m'malire ako onse.


Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsa mtima, ndi mu ukali waukulu.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.


Taona, ndimenyana ndi iwe, iwe phiri lakuononga, ati Yehova, limene liononga dziko lonse; ndipo ndidzakutambasulira iwe dzanja langa, ndipo ndidzakugubuduza iwe kumatanthwe, ndipo ndidzakuyesa iwe phiri lotenthedwa.


Musakhulupirire mau onama, kuti, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova, Kachisi wa Yehova ndi awa.


Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire, ngakhale onse okhala kunja kuno, kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova.


nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.


Atero Ambuye Yehova, Taonani, Ine ndiipidwa nao abusa, ndidzafunsa nkhosa zanga padzanja lao, ndi kuwaletsa asadyetsenso nkhosazo, ngakhale kudzidyetsa okha sadzachitanso; ndipo ndidzalanditsa nkhosa zanga pakamwa pao, zisakhale chakudya chao.


chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Taona ndidzatsutsana nawe Inedi, ndi kuchita maweruzo pakati pako pamaso pa amitundu.


Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera.


Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake mu utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako padziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa