Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 2:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo Davide anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mudzi wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono Davide adamwalira, naikidwa m'manda mu mzinda wake wa Davideyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Tsono Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 2:10
23 Mawu Ofanana  

Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mzinda wa Davide.


Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.


Pamene masiku ako akadzakwaniridwa, ndipo iwe udzagona ndi makolo ako, Ine ndidzaukitsa mbeu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m'matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.


Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa.


Ndipo atamva Hadadi ku Ejipito kuti Davide anagona ndi makolo ake, ndi kuti Yowabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu.


Ndipo Solomoni anagona ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni, nalowa ufumu m'malo mwake Abiya mwana wake.


Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.


Nagona Abiya ndi makolo ake, namuika anthu m'mzinda wa Davide; Asa mwana wake nalowa ufumu m'malo mwake.


Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.


Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni mu Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mzinda wa Davide, ndiwo Ziyoni.


Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide.


Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ake, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; nakhala mfumu m'malo mwake Ahazi mwana wake.


Nagona Ahazi ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Hezekiya mwana wake.


Nagona Yoramu ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo anyamata ake anamnyamulira pagaleta kunka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ake pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide.


Ndipo Davide anakhala m'lingamo; chifukwa chake analitcha mzinda wa Davide.


Nafa atakalamba bwino, wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anachita zabwino mu Israele, ndi kwa Mulungu, ndi kunyumba yake.


Nagona Solomoni pamodzi ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Pakutitu, Davide, m'mene adautumikira uphungu wa Mulungu m'mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;


Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa