Masalimo 87 - Buku LopatulikaYehova akonda Ziyoni Salimo la ana a Kora. Nyimbo. 1 Maziko ake ali m'mapiri oyera. 2 Yehova akonda zipata za Ziyoni koposa zokhalamo zonse za Yakobo. 3 Mzinda wa Mulungu, inu, akunenerani zakukulemekezani. 4 Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine; taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi; uyu anabadwa komweko. 5 Ndipo adzanena za Ziyoni, uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo; ndipo Wam'mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa. 6 Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu, uyu anabadwa komweko. 7 Ndipo oimba ndi oomba omwe adzati, akasupe anga onse ali mwa inu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi