Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 87:4 - Buku Lopatulika

4 Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine; taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi; uyu anabadwa komweko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndidzatchula Rahabu ndi Babiloni kwa iwo ondidziwa Ine; taonani, Filistiya ndi Tiro pamodzi ndi Kusi; uyu anabadwa komweko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Amati, “Pakati pa amene amandidziŵa, ndikutchula Rahabu ndi Babiloni. Ponena za dziko la Filistiya, Tiro ndi Etiopiya, anthu amati, ‘Uje adabadwira kumeneko.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 87:4
25 Mawu Ofanana  

Mulungu sadzabweza mkwiyo wake; athandizi odzikuza awerama pansi pa Iye.


Ku mitsinje ya ku Babiloni, kumeneko tinakhala pansi, inde tinalira, pokumbukira Ziyoni.


Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso; achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.


Akulu adzafumira ku Ejipito; Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.


Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa; munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu.


Akalonga a Zowani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


taonani, Ine, ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo padziko lino, ndi pa okhalamo ake onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo chizizwitso, ndi chotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.


Wobadwa ndi munthu iwe, uziti kwa kalonga wa Tiro, Atero Ambuye Yehova, Popeza mtima wako wadzikweza, nuti, Ine ndine Mulungu, ndikhala pa mpando wa Mulungu pakati pa nyanja, ungakhale uli munthu, wosati Mulungu, ungakhale waika mtima wako ngati mtima wa Mulungu,


Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?


Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera;


ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.


Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.


Naima iye naitana makamu a nkhondo a Israele, nanena nao, Munatulukiranji kundandalitsa nkhondo yanu? Sindine Mfilisti kodi, ndi inu anyamata a Saulo? Mudzisankhire munthu, atsikire kwa ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa