Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 87:6 - Buku Lopatulika

6 Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu, uyu anabadwa komweko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Yehova adzawerenga, polembera mitundu ya anthu, uyu anabadwa komweko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono polemba maina a mitundu yonse ya anthu, Chauta adzati, “Wakutiwakuti adabadwira ku Ziyoni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 87:6
11 Mawu Ofanana  

Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.


Afafanizidwe m'buku lamoyo, ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.


Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa mu Ziyoni, ndi iye amene atsala mu Yerusalemu adzatchedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo mu Yerusalemu;


Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.


Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; kapena kulowa m'dziko la Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.


Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mzinda, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.


Koma musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti maina anu alembedwa mu Mwamba.


Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa