Nehemiya 3:15 - Buku Lopatulika15 Ndi Chipata cha ku Kasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pamunda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumzinda wa Davide. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Ndi chipata cha kukasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumudzi wa Davide. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Salumu mwana wa Kolihoze wolamulira dera la Mizipa, adakonza Chipata cha Kasupe. Adachimanganso, naikira denga lake, zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Adamanganso khoma la Dziŵe la Sela pafupi ndi munda wa mfumu, mpaka ku makwerero otsikira potuluka mu mzinda wa Davide. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Chipata cha Kasupe chinakonzedwa ndi Saluni mwana wa Koli-Hoze, wolamulira chigawo cha Mizipa. Iye anachimanganso ndi kuyikanso denga ndiponso zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iye anakonzanso khoma la Dziwe la Siloamu limene lili pafupi ndi munda wa mfumu mpaka ku makwerero otsikira potuluka mzinda wa Davide. Onani mutuwo |