Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:14 - Buku Lopatulika

14 Ndi Chipata cha Kudzala anachikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkulu wa dziko la Betehakeremu; anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndi Chipata cha Kudzala anachikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkulu wa dziko la Betehakeremu; anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Malakiya, mwana wa Rekabu, wolamulira dera la Betehakeremu, adakonza Chipata cha Zinyalala. Adachimanganso, naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Chipata cha Zinyalala chinakonzedwa ndi Malikiya mwana wa Rekabu, wolamulira chigawo cha Beti-Hakeremu. Iye anachimanganso ndi kuyika zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:14
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Isiboseti, mwana wa Saulo anali nao amuna awiri, ndiwo atsogoleri a magulu; wina dzina lake Baana, ndi dzina la mnzake ndiye Rekabu, ndiwo ana a Rimoni wa ku Beeroti, wa ana a Benjamini, pakuti Beeroti womwe unawerengedwa wa Benjamini;


Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta.


mwana wa Mikaele, mwana wa Baaseiya, mwana wa Malikiya,


Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala;


Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.


Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.


Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa