Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:13 - Buku Lopatulika

13 Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala mu Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala m'Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Hanuni pamodzi ndi nzika za ku Zanowa adakonza Chipata cha ku Chigwa. Adachimanganso naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Adakonzanso khoma mamita 400 mpaka kukafika ku Chipata cha Zinyalala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Chipata cha ku chigwa chinakonzedwa ndi Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa. Iwo anachimanganso ndi kuyika zitseko zake ndi zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iwo anakonzanso khoma lotalika mamita 450 mpaka ku Chipata cha Zinyalala.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:13
7 Mawu Ofanana  

Ndi mkazi wake Myuda anabala Yeredi atate wa Gedori, ndi Hebere atate wa Soko, ndi Yekutiyele atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.


Uziya anamanganso nsanja mu Yerusalemu pa Chipata cha Kungodya, ndi pa Chipata cha ku Chigwa, ndi popindika linga; nazilimbikitsa.


Zanowa, Adulamu ndi midzi yao, Lakisi ndi minda yake, Azeka ndi midzi yake. Ndipo anamanga misasa kuyambira ku Beereseba mpaka chigwa cha Hinomu.


Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.


Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang'ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso.


ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu;


ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa