Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:16 - Buku Lopatulika

16 Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Pambali pa iyeyo Nehemiya, mwana wa Azibuki, wolamulira theka la dera la Betezuri, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi manda a Davide, ndi kukafika ku dziŵe lokumba ndiponso ku nyumba ya ankhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Pambali pa iyeyo, Nehemiya mwana wa Azibuki, wolamulira theka la chigawo cha Beti Zuri anakonza chigawo china mpaka kumalo oyangʼanana ndi manda a Davide, mpaka ku dziwe lokumba ndi ku nyumba ya anthu ankhondo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:16
18 Mawu Ofanana  

Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mzinda madzi, sizinalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?


Ndi mwana wa Samai ndiye Maoni; ndipo Maoni ndiye atate wa Betezuri.


ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,


Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.


Ndipo ndinapitirira kunka ku Chipata cha Chitsime, ndi ku Dziwe la Mfumu; koma popita nyama ili pansi panga panaichepera.


Ndi pambali pake anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ake akazi.


Ndi Chipata cha Kudzala anachikonza Malikiya mwana wa Rekabu, mkulu wa dziko la Betehakeremu; anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake.


Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake.


Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.


ndinadzipangira ndekha matamanda a madzi akuthirira madzi m'nkhalango momeramo mitengo;


Taonani, ndi machira a Solomoni; pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi, a mwa ngwazi za Israele.


Inu munapanganso chosungamo madzi a thamanda lakale, pakati pa malinga awiri; koma inu simunamuyang'ane iye amene anachichita icho, ngakhale kusamalira iye amene analipanga kale.


Ndipo inu munaona kuti pa mzinda wa Davide panagumuka mipata yambiri; ndipo munasonkhanitsa pamodzi madzi a m'thamanda lakunsi.


Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Tuluka tsopano kukachingamira Ahazi, iwe ndi Seari-Yasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamaliziro a mcherenje wa thamanda la pamtunda, kukhwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsalu;


Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.


Halahulu, Betezuri, ndi Gedori,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa