Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 3:17 - Buku Lopatulika

17 Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Pambali pa Nehemiyayo Alevi adakonza chigawo china. Mtsogoleri wao anali Rehumu mwana wa Bani. Pambali pa iyeyo Basabiya, wolamulira theka la dera la Keila, adakonza chigawo chake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Pambali pake Alevi anakonza chigawo china, ndipo mtsogoleri wawo anali Rehumi mwana wa Bani. Pambali pa iye Hasabiya wolamulira theka la chigawo cha Keyila anagwira ntchito ku chigawo chake.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 3:17
8 Mawu Ofanana  

A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang'anira ntchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi chimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza,


Sekaniya, Rehumu, Meremoti,


Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja.


Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkulu wa dera lina la dziko la Keila.


Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.


Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau aakulu kwa Yehova Mulungu wao.


ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa