Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 12:22 - Buku Lopatulika

22 Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ndiponso ku mzinda wa Mulungu wamoyo, ndiye kuti Yerusalemu wa Kumwamba, m'mene muli angelo osaŵerengeka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:22
49 Mawu Ofanana  

Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.


Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo. Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?


Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.


Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika.


Moyo wanga ulakalaka, inde ukomokanso ndi kufuna mabwalo a Yehova; mtima wanga ndi thupi langa zifuulira kwa Mulungu wamoyo.


Mzinda wa Mulungu, inu, akunenerani zakukulemekezani.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.


Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira chaulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi mu Yerusalemu, ndi pamaso pa akuluakulu ake.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikulu lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asiriya, ndi opirikitsidwa a m'dziko la Ejipito; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.


chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.


Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.


Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.


Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.


pamenepo padzalowa pa zipata za mzinda uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; ndipo mzinda uwu udzakhala kunthawi zamuyaya.


Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Daniele; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro.


Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.


Angakhale anatero, kuwerenga kwake kwa ana a Israele kudzanga mchenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.


Ndipo kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m'phiri la Ziyoni ndi mu Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.


Ndipo Simoni Petro anayankha nati, Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.


kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu.


ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo:


Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai, pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.


Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.


Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu;


Ndipo anati, Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala paphiri la Parani, anafumira kwa opatulika zikwizikwi; ku dzanja lamanja lake kudawakhalira lamulo lamoto.


Pakuti ndaniyo, wa zamoyo zonse adamva mau a Mulungu wamoyo wakunena ali pakati pa moto, monga ife nakhala ndi moyo?


Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; kuchokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu;


Pakuti iwo okha alalikira za ife, malowedwe athu a kwa inu anali otani; ndi kuti munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo,


Ambuye adzandilanditsa ku ntchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wake wa Kumwamba; kwa Iye ukhale ulemerero kunthawi za nthawi. Amen.


Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.


pakuti analindirira mzinda wokhala nao maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.


Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la mu Mwamba; mwa ichi Mulungu sachita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mzinda.


Pakuti pano tilibe mzinda wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


Nati Yoswa, Ndi ichi mudzadziwa kuti Mulungu wamoyo ali pakati pa inu, ndi kuti adzapirikitsa ndithu pamaso panu Akanani, ndi Ahiti, ndi Ahivi, ndi Aperizi, ndi Agirigasi, ndi Aamori, ndi Ayebusi.


Ndipo kwa iwo, Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ake zikwi makumi,


Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.


Ndipo ananditenga mu Mzimu kunka kuphiri lalikulu ndi lalitali, nandionetsa mzinda wopatulikawo, Yerusalemu, wotsika mu Mwamba kuchokera kwa Mulungu,


Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.


ndipo aliyense akachotsako pa mau a buku la chinenero ichi, Mulungu adzamchotsera gawo lake pa mtengo wa moyo, ndi m'mzinda woyerawo, ndi pa izi zilembedwa m'bukumu.


Iye wakupambana, ndidzamyesa iye mzati wa mu Kachisi wa Mulungu wanga, ndipo kutuluka sadzatulukamonso; ndipo ndidzalemba pa iye dzina la Mulungu wanga, ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, la Yerusalemu watsopano, wotsika mu Mwamba, kuchokera kwa Mulungu wanga; ndi dzina langa latsopano.


Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mau aakulu kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa