Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 5:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo tsiku lija Davide anati, Aliyense akakantha Ayebusi, aponye m'madzi opuwala ndi akhungu amene moyo wa Davide udana nao. Chifukwa chake akuti, Akhungu ndi opuwala sangalowe m'nyumbamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono tsiku limenelo Davide adati, “Aliyense wofuna kuti akakanthe Ayebusi, ayenera kudzera m'ngalande ya madzi, kuti akaphe opunduka ndi akhunguwo amene mtima wanga umadana nawo.” Nchifukwa chake amanena kuti, “Akhungu ndi opunduka sadzaloŵa m'Nyumba ya Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 5:8
5 Mawu Ofanana  

Chinkana anatero Davide anathyola linga la Ziyoni, lomwelo ndilo mzinda wa Davide.


Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.


Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa