1 Mafumu 8:1 - Buku Lopatulika1 Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni mu Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mzinda wa Davide, ndiwo Ziyoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni m'Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mudzi wa Davide, ndiwo Ziyoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake Solomoni adasonkhanitsa akuluakulu Aisraele, ndi atsogoleri onse a mafuko, akuluakulu a mabanja a Aisraele. Onsewo adasonkhana kwa mfumu Solomoni ku Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi lachipangano la Chauta, kulitulutsa m'Ziyoni, mzinda wa Davide. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Pamenepo Mfumu Solomoni inasonkhanitsa akuluakulu a Israeli, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli mu Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, Mzinda wa Davide. Onani mutuwo |
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.