Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m'Baibulo Okhudza Kudzichepetsa

110 Mau a m'Baibulo Okhudza Kudzichepetsa

Kuzindikira kufunika kwanga kwa Mulungu ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanga. Kukhala wodzichepetsa kumandithandiza kukhala pa mtendere ndi Mulungu komanso ndi anthu anzanga.

Baibulo, mu Yakobo 4:6, limati: "Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amapatsa chisomo odzichepetsa." Munthu wodzikuza amaganiza kuti amadziwa zonse ndipo sadalire Mulungu. Koma chisomo cha Mulungu chimakhala pa ife amene timadziwa kuti timamuwafuna Iye.

Popanda Mulungu, sitingathe kuchita chilichonse. Mphamvu zake zimatithandiza kukwaniritsa zolinga zathu, ndipo chifukwa cha chikondi chake, maloto athu amakwaniritsidwa. Tiyenera kukhala odzichepetsa nthawi zonse.

Chilichonse chimene tili nacho ndi chifukwa cha chifundo cha Mulungu. Iye anatiyang'ana ndi maso achifundo ndipo anatisankha kutipatsa chisomo chake. Chifukwa cha ichi, tiyenera kumpatsa ulemerero wonse chifukwa cha kukoma mtima kwake ndi ukulu wake.

Mulungu ndi wabwino ndipo ali pafupi ndi anthu amene amadzichepetsa pamaso pake ndi kumufunafuna ndi mtima wonse.




Masalimo 138:6

Angakhale Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza amdziwira kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:6

Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:5

Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 149:4

Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:10

Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:2

ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5-6

Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa. Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:2

Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru ili ndi odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:12

Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:16

Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:3-4

Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12

Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:3

Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:23

Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:4

Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:6

Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:29-30

Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:13

Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:8

Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:4

Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 9:9

Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:33

Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:2

Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:8-9

Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima, chifukwa chake adzaphunzitsa olakwa za njira. Adzawatsogolera ofatsa m'chiweruzo; ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 2:3

Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:11

Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:6

Yehova agwiriziza ofatsa; atsitsira oipa pansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:1-2

Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao, Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse. Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi. Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao, odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo. ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:9

Adzawatsogolera ofatsa m'chiweruzo; ndipo adzaphunzitsa ofatsa njira yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 6:8

Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:2

Moyo wanga udzatamanda Yehova; ofatsa adzakumva nadzakondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:18-19

Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa. Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:12

Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:29

Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:34

Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:2

Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:28-29

ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko; kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:14

ndipo anthu anga otchedwa dzina langa akadzichepetsa, nakapemphera, nakafuna nkhope yanga, nakatembenuka kuleka njira zao zoipa; pamenepo ndidzamvera mu Mwamba, ndi kukhululukira choipa chao, ndi kuchiritsa dziko lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:26-27

Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo aliyense amene akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:14

Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:5-8

Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu, ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyese cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:8

Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11

Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:7

Yehova asaukitsa, nalemeretsa; achepetsa, nakuzanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:17-18

Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye; pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:15

Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:1-4

Yang'anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo. Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu. Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso. Diso ndilo nyali ya thupi; chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowalitsidwa. Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa. Chifukwa chake ngati kuwala kumene kuli mwa inu kuli mdima, mdimawo ndi waukulu ndithu! Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma. Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala? Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? Ndipo ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi? Ndipo muderanji nkhawa ndi chovala? Tapenyetsani maluwa akuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake wonse sanavale monga limodzi la amenewa. Koma iwe popatsa mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe chimene lichita dzanja lako lamanja; Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wakuthengo, ukhala lero, ndi mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono? Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? Kapena, Tidzamwa chiyani? Kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake. kotero kuti mphatso zako zachifundo zikhale zam'tseri; ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:20

Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:3

Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali chabe, adzinyenga yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 22:29

Anthu akakugwetsa pansi, udzati, Adzandikweza; ndipo adzapulumutsa wodzichepetsayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:11

Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:14-15

Chifukwa chake, ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake. Pakuti ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:3

osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:30

Ngati ndiyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira ndi za kufooka kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:23-24

pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:12-13

Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:10-12

Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Khristu. Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:26

Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 9:23-24

Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake; koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:4-5

Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 34:27

popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:6-7

Usadzitame pamaso pa mfumu, ngakhale kuima m'malo mwa akulu. Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, amene maso ako anamuona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1-2

Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha. Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake. Ndiponso, Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse; ndipo anthu onse amtamande. Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera. Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera. Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake. Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu, kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera. Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu. Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito, mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu; Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:30

Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:4

Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza, ndi nyali ya oipa, zili tchimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 5:11

kuika opeputsidwa pamalo ponyamuka, kuti iwo a maliro akwezedwe kosatekeseka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:23

amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-5

Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso. Inde chomwecho pa zipatso zao mudzawazindikira iwo. Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika. Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu. Ndipo panakhala pamene Yesu anatha mau amenewa, makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao. Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 4:6

Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:21

ndi kumverana wina ndi mnzake m'kuopa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:23

Wosauka amadandaulira; koma wolemera ayankha mwaukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:3

Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:17

Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:13

Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadze kudzaitana olungama, koma ochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:10

Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:1-4

Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe. Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse. Pakuti Iye wakuti, Usachite chigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo. Lankhulani motero, ndipo chitani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu. Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro. Chipindulo chake nchiyani, abale anga, munthu akanena, Ndili nacho chikhulupiriro, koma alibe ntchito? Kodi chikhulupirirocho chikhoza kumpulumutsa? Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani? Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nacho ntchito, chikhala chakufa m'kati mwakemo. Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndili nazo ntchito; undionetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m'ntchito zanga. Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; uchita bwino; ziwanda zikhulupiriranso, ndipo zinthunthumira. Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa; Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe? Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe? Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina? Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa. ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga; kodi simunasiyanitse mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:10

Chotero inunso m'mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:9

Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 9:20-21

Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero? Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Njira ya chitsiru njolungama pamaso pakepake; koma wanzeru amamvera uphungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:7

Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:6

podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:8-9

Tikati kuti tilibe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe choonadi. Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:1-2

Ngati tsono muli chitonthozo mwa Khristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni, kuti m'dzina la Yesu bondo lililonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi padziko, ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate. Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu. Chitani zonse kopanda madandaulo ndi makani, kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi, akuonetsera mau a moyo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira nao m'tsiku la Khristu, kuti sindinathamange chabe, kapena kugwiritsa ntchito chabe. Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse; momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine. Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu. kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:17

Wosunga mwambo ali m'njira ya moyo; koma wosiya chidzudzulo asochera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11

ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:15

Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:27-28

Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:15-16

Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:19

Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:17

Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 69:32

Ofatsa anachiona, nakondwera, ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:4-5

Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:38-39

Ndipo iye amene satenga mtanda wake, natsata pambuyo panga, sayenera Ine. Iye amene apeza moyo wake, adzautaya; ndi iye amene ataya moyo wake, chifukwa cha Ine, adzaupeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:36-37

Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa. Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:15

Mukadanena inu, Akalola Ambuye, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:13

Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ndi mtima waulemu ndimabwera pamaso panu kukulambirani ndi kukupatsani ulemerero, ndikudziwa kuti ndinu mphamvu ya moyo wanga, amene amandilimbitsa ndi kundithandiza m'masautso anga onse. Mulungu wanga, ndikukuthokozani chifukwa cha chikondi chanu chosatha, chifukwa mwandikomera mtima ndi kundidzaza ndi chisomo chanu. Ndikufuna kukhala pamaso panu nthawi zonse, kuti thupi langa lonse likutamandeni ndi kukupatsani ulemerero wonse. Palibe chomwe ndingathe kuchita ndi luso langa, palibe chomwe ndingadzitamandire nacho, chifukwa ndimakuzindikirani m'njira zanga zonse ndipo ndikudziwa kuti chilichonse chimene ndili ndi chifukwa cha inu. Musalole, Mulungu, kuti mtima wanga udzale ndi kudzikuza, munditsuke kuunyinji wonse umene ukufuna kukhala mkati mwanga, munditeteze ku kudzikuza konse, pangani mtima wanga kukhala wolungama ndi womvera pamaso panu kuti ndikhale wodzichepetsa pamaso panu nthawi zonse, chifukwa mawu anu amati mudzaseka onse akuseka, ndipo odzichepetsa mudzawapatsa chisomo. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa