Luka 18:14 - Buku Lopatulika14 Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.” Onani mutuwo |
koma podziwa kuti munthu sayesedwa wolungama pa ntchito ya lamulo, koma mwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu, ifedi tinakhulupirira kwa Khristu Yesu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro cha Khristu, ndipo si ndi ntchito za lamulo; pakuti palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo.