Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 22:26 - Buku Lopatulika

26 Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Koma sipadzatero ndi inu; komatu iye ali wamkulu mwa inu, akhale ngati wamng'ono; ndi iye ali woyamba, akhale ngati wotumikira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Koma pakati pa inu zisamatero ai. Kwenikweni wamkulu mwa inu azikhala ngati wamng'ono mwa onse, ndipo mtsogoleri azikhala ngati wotumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira.

Onani mutuwo Koperani




Luka 22:26
10 Mawu Ofanana  

Sikudzakhala chomwecho kwa inu ai; koma aliyense amene akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu;


Koma mwa inu sikutero ai; koma aliyense amene afuna kukhala wamkulu mwa inu adzakhala mtumiki wanu;


Ndipo m'mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.


Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.


Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.


osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.


Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa