Numeri 34 - Buku LopatulikaMalire a dziko la Kanani 1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, 2 Uza ana a Israele, nunene nao, Mutalowa m'dziko la Kanani, ndilo dziko logwera inu, likhale cholowa chanu, dziko la Kanani monga mwa malire ake, 3 dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa; 4 ndi malire anu adzapinda kuchokera kumwera kunka pokwera Akarabimu, ndi kupitirira ku Zini; ndi kutuluka kwake adzachokera kumwera ku Kadesi-Baranea, nadzatuluka kunka ku Hazara-Adara, ndi kupita kunka ku Azimoni; 5 ndipo malirewo adzapinda ku Azimoni kunka ku mtsinje wa Ejipito, ndi kutuluka kwao adzatuluka kunyanja. 6 Kunena za malire a kumadzulo Nyanja Yaikulu ndiyo malire anu; ndiyo malire anu a kumadzulo. 7 Malire anu a kumpoto ndiwo: kuyambira ku Nyanja Yaikulu mulinge kuphiri la Hori: 8 kuchokera kuphiri la Hori mulinge polowera Hamati; ndipo kutuluka kwake kwa malire kudzakhala ku Zedadi. 9 Ndipo malirewo adzatuluka kunka ku Zifuroni, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Hazara-Enani; ndiwo malire anu a kumpoto. 10 Ndipo mudzilembere malire a kum'mawa ochokera ku Hazara-Enani kunka ku Sefamu; 11 ndi malire adzatsika ku Sefamu kunka ku Ribula, kum'mawa kwa Aini; ndipo malire adzatsika, nadzafikira mbali ya nyanja ya Kinereti kum'mawa, 12 ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga. 13 Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu; 14 popeza fuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi hafu la fuko la Manase lalandira cholowa chao; 15 mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa. 16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, 17 Maina a amunawo adzakugawirani dziko likhale cholowa chanu, ndi awa: Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni. 18 Muwatengenso akalonga, kalonga mmodzi ku fuko limodzi, agawe dziko likhale cholowa chao. 19 Maina a amunawo ndiwo: wa fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune. 20 Wa fuko la ana a Simeoni, Semuele mwana wa Amihudi. 21 Wa fuko la Benjamini, Elidadi mwana wa Kisiloni. 22 Wa fuko la ana a Dani, kalonga Buki mwana wa Yogili. 23 Wa ana a Yosefe; wa fuko la ana a Manase, kalonga Haniyele mwana wa Efodi. 24 Wa fuko la ana a Efuremu, kalonga Kemuwele mwana wa Sifutani. 25 Wa fuko la ana a Zebuloni, kalonga Elizafani mwana wa Paranaki. 26 Wa fuko la ana a Isakara, kalonga Palatiele mwana wa Azani. 27 Wa fuko la ana a Asere, kalonga Ahihudi mwana wa Selomi. 28 Wa fuko la ana a Nafutali, kalonga Pedahele mwana wa Amihudi. 29 Iwo ndiwo amene Yehova analamulira agawire ana a Israele cholowa chao m'dziko la Kanani. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi