Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 34:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Mose anauza ana a Israele, nati, Ili ndi dzikoli mudzalandira ndi kuchita maere, limene Yehova analamulira awapatse mafuko asanu ndi anai ndi hafu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mose adalamula Aisraele kuti, “limeneli ndilo dziko limene mudzalandira mwamaere kuti likhale choloŵa chanu, limene Chauta walamula kuti lipatsidwe kwa mafuko asanu ndi anai ndi theka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 34:13
10 Mawu Ofanana  

Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m'litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ake onse pozungulira pake.


Chifukwa chake udzasowa woponya chingwe chamaere m'msonkhano wa Yehova.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


ndi malire adzatsika ku Yordani, ndi kutuluka kwake kudzakhala ku Nyanja ya Mchere; ili ndili dziko lanu monga mwa malire ake polizinga.


Pamalo ponse padzapondapo phazi lanu ndi panu, kuyambira chipululu ndi Lebanoni, kuyambira pamtsinjewo, mtsinje wa Yufurate, kufikira nyanja ya m'tsogolo, ndiwo malire anu.


Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi hafu la fuko la Manase, dziko ili likhale cholowa chao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa