Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 34:14 - Buku Lopatulika

14 popeza fuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi hafu la fuko la Manase lalandira cholowa chao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 popeza fuko la ana a Rubeni monga mwa nyumba za makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi monga mwa nyumba za makolo ao, adalandira, ndi fuko la hafu la Manase lalandira cholowa chao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Fuko la ana a Rubeni mwa mabanja a makolo ao, ndi fuko la ana a Gadi mwa mabanja a makolo ao, pamodzi ndi theka la fuko la Manase, adalandira kale choloŵa chao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 34:14
8 Mawu Ofanana  

Koma mukapanda kutero, taonani, mwachimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti tchimo lanu lidzakupezani.


Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi hafu la fuko la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi mizinda yake m'malire mwao, ndiyo mizinda ya dziko lozungulirako.


mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.


Ndipo anadzisankhira gawo loyamba, popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira; ndipo anadza ndi mafumu a anthu, anachita chilungamo cha Yehova, ndi maweruzo ake ndi Israele.


kupirikitsa amitundu aakulu ndi amphamvu oposa inu pamaso panu, kukulowetsani ndi kukupatsani dziko lao likhale cholowa chanu, monga lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa