Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 34:3 - Buku Lopatulika

3 dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 dera lanu la kumwera lidzakhala lochokera ku chipululu cha Zini, kutsata m'mphepete mwa Edomu, ndi malire anu a kumwera adzakhala ochokera ku malekezero a Nyanja ya Mchere kum'mawa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chigawo chakumwera cha dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini kulambalala malire a Edomu. Malire anu akumwera ayambira kuvuma, kumathero a Nyanja ya Mchere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 34:3
9 Mawu Ofanana  

Onse amenewo anadziphatikana pa chigwa cha Sidimu (pamenepo ndi pa Nyanja ya Mchere).


Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.


Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.


Pamenepo anati kwa ine, Madzi awa atulukira kudera la kum'mawa, natsikira kuchidikha, nayenda kunyanja; atathira kunyanja akonzeka madzi ake.


Pamenepo anakwerako, nazonda dziko kuyambira chipululu za Zini kufikira Rehobu, polowa ku Hamati.


Kuyambira chipululu, ndi Lebanoni uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Yufurate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira Nyanja Yaikulu ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.


pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa