Eksodo 6 - Buku Lopatulika1 Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake. 2 Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA: 3 ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwike kwa iwo ndi dzina langa YEHOVA. 4 Ndipo ndinakhazikitsanso nao chipangano changa, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo. 5 Ndamvanso kubuula kwa ana a Israele, amene Aejipito awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa. 6 Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu; 7 ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito. 8 Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova. 9 Ndipo Mose ananena chomwecho ndi ana a Israele; koma sanamvere Mose chifukwa cha kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera. 10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, 11 Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito, kuti alole ana a Israele atuluke m'dziko lake. 12 Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula? 13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito. Chibadwidwe cha Mose ndi Aroni 14 Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni. 15 Ndi ana aamuna a Simeoni ndiwo: Yemuwele, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo mwana wa mkazi wa Mkanani; amenewo ndiwo mabanja a Simeoni. 16 Ndipo maina a ana aamuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Geresoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. 17 Ana aamuna a Geresoni ndiwo: Libini ndi Simei, mwa mabanja ao. 18 Ndi ana aamuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu. 19 Ndipo ana aamuna a Merari ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao. 20 Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. 21 Ndi ana aamuna a Izihara ndiwo: Kora ndi Nefegi, ndi Zikiri. 22 Ndi ana aamuna a Uziyele ndiwo: Misaele, ndi Elizafani, ndi Sitiri. 23 Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara. 24 Ndipo ana aamuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora. 25 Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao. 26 Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao. 27 Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele mu Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa. Mulungu ampangira Mose 28 Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Ejipito, 29 Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova; lankhula ndi Farao mfumu ya Aejipito zonsezi Ine ndizinena nawe. 30 Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndili wa milomo yosadula ndipo Farao adzandimvera bwanji? |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi