Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 6:14 - Buku Lopatulika

14 Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amene ndiwo mabanja a Rubeni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Naŵa atsogoleri a mabanja a makolo ao. Ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele, anali aŵa: Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Ameneŵa ndiwo a m'banja la Rubeni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 6:14
17 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Levi: Geresoni, Kohati, ndi Merari.


Ndi ana aamuna a Rubeni: Hanoki, ndi Palu, ndi Hezironi, ndi Karimi.


Ndipo akulu a nyumba za makolo ao ndi awa: Efere, ndi Isi, ndi Eliyele, ndi Aziriele, ndi Yeremiya, ndi Hodaviya, ndi Yadiyele, anthu amphamvu ndithu, anthu omveka, akulu a nyumba za makolo ao.


ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele: Hanoki, ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi.


Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Refaya, ndi Yeriyele, ndi Yamai, ndi Ibisamu, ndi Semuele, akulu a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao, masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.


Ndi ana a Bela: Eziboni, ndi Uzi, ndi Uziyele, ndi Yerimoti, ndi Iri, asanu; akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu, owerengedwa m'mabuku a chibadwidwe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza makumi atatu ndi anai.


Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akulu a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kunka ku Manahati,


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito.


Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao.


nasonkhanitsa khamu lonse tsiku loyamba la mwezi wachiwiri, ndipo iwo anawakumbira magwero ao kutchula mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao, ndi kuwerenga maina kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu mmodzimmodzi.


Ana aamuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;


Ndipo Mose anapatsira fuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao.


Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordani ndi malire ake. Ndicho cholowa cha ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, mizinda yake ndi midzi yake.


Ndipo awa ndi maiko ana a Israele anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, anawagawira.


Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa