Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 6:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma Chauta adalamula Mose ndi Aroni kuti akauze Aisraele ndi Farao mfumu ya ku Ejipito, kuti Aisraelewo ayenera kutuluka m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndipo Yehova analamula Mose ndi Aaroni kuti awuze Aisraeli ndi Farao mfumu ya Igupto kuti Aisraeli ayenera kutuluka mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 6:13
14 Mawu Ofanana  

Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse.


Koma Mose ananena pamaso pa Yehova, ndi kuti, Onani, ana a Israele sanandimvere ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula?


Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.


Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao.


numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao.


namuikira manja ake, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose.


nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.


Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;


Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.


Ndikulamulira pamaso pa Mulungu, wozipatsa zinthu zonse moyo, ndi Khristu Yesu, amene anachitira umboni chivomerezo chabwino kwa Pontio Pilato;


Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo;


Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.


Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ake ndi ufumu wake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa