Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 6:27 - Buku Lopatulika

27 Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele mu Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aejipito, awatulutse ana a Israele m'Ejipito; Mose ndi Aroni amenewa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Ameneŵa ndiwo ankauza Farao mfumu ya ku Ejipito kuti atulutse Aisraele ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Mose ndi Aaroni ndiwo amene anayankhula ndi Farao mfumu ya Igupto kuti atulutse Aisraeli mu Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 6:27
12 Mawu Ofanana  

Anatuma Mose mtumiki wake, ndi Aroni amene adamsankha.


Munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa, ndi dzanja la Mose ndi Aroni.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m'dziko la Ejipito wadziipsa;


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israele, ndi za Farao mfumu ya Aejipito, kuti atulutse ana a Israele m'dziko la Ejipito.


Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Tulutsani ana a Israele m'dziko la Ejipito mwa makamu ao.


Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Ejipito,


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka.


Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.


Pamenepo ndinatuma Mose ndi Aroni, ndipo ndinasautsa Aejipito, monga ndinachita pakati pake; ndipo nditatero ndinakutulutsani.


Ndipo Samuele ananena ndi anthuwo, Yehova ndiye amene anaika Mose ndi Aroni, natulutsanso makolo anu m'dziko la Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa