Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 6:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Aroni adakwatira Eliseba mwana wa Aminadabu, ndipo mlongo wake anali Nasoni. Eliseba adabala Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Aaroni anakwatira Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wa Nasoni ndipo Iye anabereka Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 6:23
19 Mawu Ofanana  

Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda;


Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.


Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;


Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri anakwerako;


Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi paguwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;


Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa.


Wa Yuda, Nasoni mwana wa Aminadabu.


Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.


Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wake, nukwere nao m'phiri la Hori;


Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.


ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni; ndi Nasoni anabala Salimoni;


Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti.


Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika paphiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa