Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.
Masalimo 6:4 - Buku Lopatulika Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bwerani, Inu Chauta, mudzandilanditse. Mundipulumutse chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. |
Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.
Ndidzachita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti, pokhala ndi chisoni m'mtima mwanga tsiku lonse? Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?
Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;
Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.
Koma ine, pemphero langa lili kwa Inu, Yehova, m'nyengo yolandirika; Mulungu, mwa chifundo chanu chachikulu, mundivomereze ndi choonadi cha chipulumutso chanu.
Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?
Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu; suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,
Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.
Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.
Mulungu wanga, tcherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mzinda udatchedwawo dzina lanu; pakuti dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, chifukwa cha ntchito zathu zolungama, koma chifukwa cha zifundo zanu zochuluka.
Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?
kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.