Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 80:14 - Buku Lopatulika

14 Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu; suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu; suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mutembenukirenso kwa ife, Inu Mulungu Wamphamvuzonse, muyang'ane Inu okhala kumwamba, ndipo muwone. Samalani mpesawo,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse! Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone! Uyangʼanireni mpesa umenewu,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 80:14
10 Mawu Ofanana  

Yehova apenyerera m'mwamba; aona ana onse a anthu.


Ndipo ukuzingeni msonkhano wa anthu; ndipo pamwamba pao mubwerere kunka kumwamba.


Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.


kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona.


Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.


Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?


Zikatha izo ndidzabwera, ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chinagwa; ndidzamanganso zopasuka zake, ndipo ndidzachiimikanso:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa