Masalimo 13 - Buku LopatulikaMunkhawa athawira Mulungu namkhulupirira Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. 1 Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti? 2 Ndidzachita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti, pokhala ndi chisoni m'mtima mwanga tsiku lonse? Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti? 3 Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga. Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa; 4 kuti anganene mdani wanga, Ndamgonjetsa; ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine. 5 Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu. 6 Ndidzaimbira Yehova, pakuti anandichitira zokoma. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi