Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 13:1 - Buku Lopatulika

1 Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Kodi mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzandiiŵala mpaka muyaya? Kodi mudzandibisira nkhope yanu nthaŵi zonse?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 13:1
15 Mawu Ofanana  

Mubisiranji nkhope yanu, ndi kundiyesa mdani wanu?


Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika.


Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.


Mubisiranji nkhope yanu, ndi kuiwala kuzunzika ndi kupsinjika kwathu?


Moyo wanganso wanthunthumira kwakukulu; ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?


Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?


Yehova, Mulungu wa makamu, mudzakwiyira pemphero la anthu anu kufikira liti?


Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse? Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo?


Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?


Mutikhutitse nacho chifundo chanu m'mawa; ndipo tidzafuula mokondwera ndi kukondwera masiku athu onse.


koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.


Bwanji mutiiwala chiiwalire, ndi kutisiya masiku ambirimbiri.


Pamenepo ndidzawapsera mtima tsiku ilo, ndipo ndidzawataya, ndi kuwabisira nkhope yanga, ndipo adzathedwa, ndi zoipa ndi zovuta zambiri zidzawafikira; kotero kuti adzati tsiku lija, Sizitifikira kodi zoipa izi popeza Mulungu wathu sakhala pakati pa ife?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa