Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 17:13 - Buku Lopatulika

13 Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Dzambatukani, Inu Chauta, mukumane nawo ndi kuŵagonjetsa. Mundipulumutse ndi lupanga lanu kwa anthu oipawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi; landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 17:13
16 Mawu Ofanana  

Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu; musaiwale ozunzika.


Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu; pakuti anaswa chilamulo chanu.


Landitsani moyo wanga kulupanga; wokondedwa wanga kumphamvu ya galu,


Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.


Galamukani, mugoneranji, Ambuye? Ukani, musatitaye chitayire.


Ukani, tithandizeni, tiomboleni mwa chifundo chanu.


Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo.


Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?


Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.


Iwe Asiriya chibonga cha mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lake muli ukali wanga!


Achokera m'dziko lakutali, kumalekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wake, kuti aononge dziko lonse.


Kodi iwe sunamve, kuti ndinachita ichi kale, ndi kuchikonza nthawi zakale? Tsopano Ine ndachikwaniritsa, kuti iwe ukapasule mizinda yamalinga, isanduke miunda.


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


kuti achite zilizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa