Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 17:14 - Buku Lopatulika

14 kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Inu Chauta, ndi dzanja lanu mundilanditse kwa adani, kwa anthu amene moyo wao umangosamala zapansipano. Muŵalange ndi zoŵaŵa zimene mudaŵasungira. Nawonso ana awo akhale nazo zambiri, ndipo iwowo asiyireko ana aonso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere, kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno. Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu; ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri, ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 17:14
21 Mawu Ofanana  

Mahema a achifwamba akhala mumtendere, ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima; amene Mulungu amadzazira dzanja lao.


Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse; kuti dzanja la Yehova lichita ichi?


Pakuti chomsamalitsa nyumba yake nchiyani, atapita iye, chiwerengo cha miyezi yake chitadulidwa pakati?


Angakhale Iye adadzaza nyumba zao ndi zabwino; koma uphungu wa oipa unditalikira.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Tapenyani, oipa ndi awa; ndipo pokhazikika chikhazikikire aonjezerapo pa chuma chao.


ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika;


Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.


Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.


Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.


Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.


Ine ndawapatsa iwo mau anu; ndipo dziko lapansi, linadana nao, chifukwa sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.


Ndipo ananena nao, Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera Kumwamba; inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi.


Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m'tsiku lakupha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa