Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 90:13 - Buku Lopatulika

13 Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Bwerani, Yehova; kufikira liti? Ndipo alekeni atumiki anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Lezani mtima, Inu Chauta. Nanga mudzatikwiyira mpaka liti? Achitireni chifundo atumiki anu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Achitireni chifundo atumiki anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 90:13
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anawakumbukira chipangano chake, naleza monga mwa kuchuluka kwa chifundo chake.


Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake, koma adzaleka atumiki ake.


Pakuti muimfa m'mosakumbukira Inu; m'mandamo adzakuyamikani ndani?


Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?


Bwererani, tikupemphani, Mulungu wa makamu; suzumirani muli m'mwamba, nimupenye, ndi kuzonda mpesa uwu,


ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka, ndi mphanda munadzilimbikitsira.


Mudzabisala kosatha kufikira liti, Yehova; ndi kuzaza kwanu kudzatentha ngati moto kufikira liti?


Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.


Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake.


Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.


Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawachitira chisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku cholowa chake, ndi yense kudziko lake.


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova.


Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.


Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.


Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.


Ndi pakupumula ili anati, Bwerani Yehova kwa zikwizikwi za Israele.


Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa